Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 7:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo anthu onse ndi amisonkho omwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo anthu onse ndi amisonkho omwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Anthu onse, ndi okhometsa msonkho omwe, adamva mau a Yohane, ndipo pakubatizidwa ndi Yohaneyo adavomereza kuti Mulungu ngwolungama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Anthu onse, ngakhale amisonkho, atamva mawu a Yesu, anavomereza kuti njira ya Mulungu ndi yolondola, chifukwa anabatizidwa ndi Yohane.

Onani mutuwo Koperani




Luka 7:29
15 Mawu Ofanana  

Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.


Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?


Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.


Ndipo amisonkho omwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizichita chiyani?


Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkulu woposa Yohane; koma iye amene ali wamng'ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye.


Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ana ake onse.


Iyeyo anaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;


Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m'chiyani? Ndipo anati, Mu ubatizo wa Yohane.


Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonje ku chilungamo cha Mulungu.


Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.


Ndipo ndinamva mngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, amene muli, nimunali, Woyera Inu, chifukwa mudaweruza kotero;


Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa