Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 7:28 - Buku Lopatulika

28 Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkulu woposa Yohane; koma iye amene ali wamng'ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkulu woposa Yohane; koma iye amene ali wamng'ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 “Ndithu ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi yemwe woposa Yohane. Komabe ngakhale amene ali wamng'onong'ono mu Ufumu wa Mulungu amampambana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Ine ndikukuwuzani kuti pakati pa obadwa kuchokera mwa mkazi palibe wina wamkulu kuposa Yohane; komabe amene ali wamngʼono mu ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iye.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 7:28
13 Mawu Ofanana  

Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa mkazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.


Ndipo masiku aja anadza Yohane Mbatizi, nalalikira m'chipululu cha Yudeya,


Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula zingwe za nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:


Uyu ndi iye amene kunalembedwa za iye, Ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere, amene adzakukonzera njira yako pamaso pako.


Ndipo anthu onse ndi amisonkho omwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.


Amene aliyense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira Iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa