Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
Luka 24:4 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, m'mene anathedwa nzeru nacho, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atavala zonyezimira; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, m'mene anathedwa nzeru nacho, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atavala zonyezimira; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akadali othedwa nzeru choncho pa zimenezo, adangoona anthu aŵiri ovala zovala zonyezimira ataimirira pafupi ndi iwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene iwo ankadabwa za zimenezi, mwadzidzidzi, amuna awiri ovala zovala zonyezimira kwambiri anayimirira pambali pawo. |
Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
Ndipo pamene analowa m'manda, anaona mnyamata alikukhala kumbali ya kudzanja lamanja, wovala mwinjiro woyera; ndipo iwo anadabwa.
Ndipo mngelo wa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha aakulu.
ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?
Ndipo pakukhala iwo chipenyerere kumwamba pomuka Iye, taonani, amuna awiri ovala zoyera anaimirira pambali pao;
Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga. Ndipo maunyolo anagwa kuchoka m'manja mwake.
Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.