Ndilenga chipatso cha milomo, Mtendere, mtendere kwa iye amene ali kutali, ndi kwa iye amene ali chifupi, ati Yehova; ndipo ndidzamchiritsa iye.
Luka 10:5 - Buku Lopatulika Ndipo m'nyumba iliyonse mukalowamo muyambe mwanena, Mtendere ukhale pa nyumba iyi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'nyumba iliyonse mukalowamo muthange mwanena, Mtendere ukhale pa nyumba iyi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kunyumba kulikonse kumene mukaloŵe, muyambe mwanena kuti, ‘Mtendere ukhale m'nyumba muno.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Mukamalowa mʼnyumba, poyamba nenani kuti, ‘Mtendere pa nyumba ino.’ |
Ndilenga chipatso cha milomo, Mtendere, mtendere kwa iye amene ali kutali, ndi kwa iye amene ali chifupi, ati Yehova; ndipo ndidzamchiritsa iye.
Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalonjere munthu panjira.
Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m'menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu.
Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu.
Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse)
ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi;
ndipo muzitero kwa wodalayo, Mtendere ukhale pa inu, mtendere ukhalenso pa nyumba yanu, ndi mtendere ukhale pa zonse muli nazo.