Luka 1:54 - Buku Lopatulika Anathangatira Israele mnyamata wake, kuti akakumbukire chifundo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anathangatira Israele mnyamata wake, kuti akakumbukire chifundo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wadzathandiza anthu ake Aisraele, pokumbukira chifundo chake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anathandiza mtumiki wake Israeli, pokumbukira chifundo chake. |
Anakumbukira chifundo chake ndi chikhulupiriko chake kunyumba ya Israele; malekezero onse a dziko lapansi anaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Kumbukira zinthu izi, Yakobo; ndi Israele, pakuti iwe ndiwe mtumiki wanga; ndakuumba, iwe ndiwe mtumiki wanga, Israele, sindidzakuiwala.
Kodi Efuremu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? Nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; chifukwa chake mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamchitiradi chifundo, ati Yehova.
Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.
Mudzapatsa kwa Yakobo choonadi, ndi kwa Abrahamu chifundo chimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe.