Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 7:20 - Buku Lopatulika

20 Mudzapatsa kwa Yakobo choonadi, ndi kwa Abrahamu chifundo chimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Mudzapatsa kwa Yakobo choonadi, ndi kwa Abrahamu chifundo chimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Mudzaonetsa kukhulupirika kwanu kwa Yakobe, ndi chikondi chanu chosasinthika kwa Abrahamu, monga mudalonjezera molumbira kwa makolo athu kuyambira pa masiku amakedzana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Mudzakhala wokhulupirika kwa Yakobo, ndi kuonetsa chifundo chanu kwa Abrahamu, monga munalonjeza molumbira kwa makolo athu masiku amakedzana.

Onani mutuwo Koperani




Mika 7:20
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga.


sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri.


Taonani, ndidzautengera moyo ndi kuuchiritsa, ndi kuwachiritsa; ndipo ndidzawaululira iwo kuchuluka kwa mtendere ndi zoona.


Ndipo kudzakhala, chifukwa cha kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwachita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani chipangano ndi chifundo chimene analumbirira makolo anu;


koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m'nyumba ya ukapolo, m'dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, chifukwa Yehova akukondani, ndi chifukwa cha kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa