Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nahumu 1:1 - Buku Lopatulika

1 Katundu wa Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Katundu wa Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Uwu ndi uthenga wonena za mzinda wa Ninive. Uthengawu ukufotokoza za zimene Nahumu wa ku Elikosi adaziwona m'masomphenya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Uthenga wonena za Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.

Onani mutuwo Koperani




Nahumu 1:1
19 Mawu Ofanana  

M'dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Asiriya, namanga Ninive, ndi mzinda wa Rehoboti, ndi Kala,


Nachoka Senakeribu mfumu ya Asiriya, namuka, nabwerera, nakhala ku Ninive.


Iwe Asiriya chibonga cha mkwiyo wanga, ndodo m'dzanja lake muli ukali wanga!


Katundu wa Babiloni, amene anamuona Yesaya mwana wa Amozi.


Chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira katundu amene analipo.


Katundu wa Mowabu. Pakuti usiku umodzi Ari wa ku Mowabu wapasuka, nakhala chabe; usiku umodzi Kiri wa Mowabu wapasuka, nakhala chabe.


Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake.


Katundu wa chipululu cha kunyanja. Monga akamvulumvulu a kumwera apitirira, kufumira kuchipululu kudziko loopsa.


Katundu wa chigwa cha masomphenya. Mwatani kuti mwakwera nonsenu pamatsindwi?


Katundu wa Tiro. Kuwani, inu ngalawa za Tarisisi; chifukwa wapasudwa, kulibenso nyumba, kulibe polowera; kuchokera kudziko la Kitimu kwavumbulutsidwa kwa iwo.


Aneneri amene analipo kale ndisanakhale ine, nimusanakhale inu, ananenera maiko ambiri, ndi mafumu aakulu, za nkhondo, ndi za choipa, ndi za mliri.


Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukuluwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga.


Koma Ninive wakhala chiyambire chake ngati thamanda lamadzi; koma athawa. Imani, Imani! Ati, koma palibe wocheuka.


Katundu adamuona mneneri Habakuku


Ndipo adzatambasulira dzanja lake kumpoto nadzaononga Asiriya, nadzasanduliza Ninive akhale bwinja, wouma ngati chipululu.


Katundu wa mau a Yehova padziko la Hadaraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pake; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israele;


Katundu wa mau a Yehova wa kwa Israele mwa Malaki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa