Mau a pakamwa pake ndiwo opanda pake ndi onyenga, waleka kuzindikira ndi kuchita bwino.
Hoseya 8:3 - Buku Lopatulika Israele wachitaya chokoma, mdani adzamlondola. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Israele wachitaya chokoma, mdani adzamlondola. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Aisraele akana zabwino. Nchifukwa chake adani ao adzaŵapirikitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Israeli wakana zabwino; mdani adzamuthamangitsa. |
Mau a pakamwa pake ndiwo opanda pake ndi onyenga, waleka kuzindikira ndi kuchita bwino.
Otilondola anaposa ziombankhanga za m'mlengalenga m'liwiro lao, anatithamangitsa pamapiri natilalira m'chipululu.
Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe.
Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang'amba ching'ambire nasunga mkwiyo wake chisungire;
Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.