Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo padziko lapansi, naphwa madzi;
Genesis 9:10 - Buku Lopatulika ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, zouluka, ng'ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zotuluka m'chingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, zouluka, ng'ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zotuluka m'chingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndi zamoyo zonse, mbalame, zoŵeta, nyama zakuthengo, ndi zina zonse zimene zidatuluka nanu m'chombo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pamodzi ndi zamoyo zonse, mbalame, ziweto ndi nyama zonse za kuthengo, ndi zonse zimene zinatuluka mʼchombo pamodzi ndi iwe. |
Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo padziko lapansi, naphwa madzi;
zinyama zonse, zokwawa zonse, zouluka zonse, ndi zonse zokwawa padziko lapansi, monga mwa mitundu yao, zinatuluka m'chingalawamo.
Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamalizidwanso konse ndi madzi a chigumula; ndipo sikudzakhalanso konse chigumula cha kuononga dziko lapansi.
Ndipo Ine, taonani, Ine ndikhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu, ndi mbeu zanu pambuyo panu;
ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?