Genesis 8:9 - Buku Lopatulika koma njiwayo siinapeze popondapo phazi lake, nibwera kwa iye kuchingalawako, pakuti madzi analipo padziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m'chingalawamo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma njiwayo siinapeza popondapo phazi lake, nibwera kwa iye kuchingalawako, pakuti madzi analipo pa dziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m'chingalawamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma popeza kuti madzi anali akadalipobe pa dziko lonse, nkhundayo idabwerera, chifukwa idaasoŵa potera. Nowa adatambalitsa dzanja kunja, nailoŵetsanso m'chombo muja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali. |
Ndipo anatulutsa njiwa imchokere, kuti aone kapena madzi anaphwa pamwamba padziko lapansi;
Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, aliyense m'mphulupulu zake.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m'maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.