Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 8:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 koma njiwayo siinapeze popondapo phazi lake, nibwera kwa iye kuchingalawako, pakuti madzi analipo padziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m'chingalawamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 koma njiwayo siinapeza popondapo phazi lake, nibwera kwa iye kuchingalawako, pakuti madzi analipo pa dziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m'chingalawamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma popeza kuti madzi anali akadalipobe pa dziko lonse, nkhundayo idabwerera, chifukwa idaasoŵa potera. Nowa adatambalitsa dzanja kunja, nailoŵetsanso m'chombo muja.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 8:9
8 Mawu Ofanana  

Choncho anadikirabe masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatulutsanso nkhundayo mʼchombo muja.


Kenaka anatulutsa nkhunda kuti aone ngati madzi aphwa pa dziko.


Pumula iwe moyo wanga, pakuti Yehova wakuchitira zokoma.


“Kodi ndi zayani izo zikuwuluka ngati mitambo, ngati kapena nkhunda zobwerera ku zisa zawo?


Onse amene adzapulumuka ndi kumakakhala ku mapiri, azidzalira ngati nkhunda za ku zigwa. Aliyense azidzabuwula chifukwa cha machimo ake.


“Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.


“Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”


Pakati pa mitundu ya anthu imeneyi simudzapeza mpata, popanda malo woti nʼkuyikapo phazi. Kumeneko Yehova adzakupatsani moyo wa nkhawa, maso otopa ndi chiyembekezo, ndi mtima wosakhazikika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa