Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la chingalawa limene analipanga:
Genesis 8:7 - Buku Lopatulika ndipo anatulutsa khwangwala, ndipo anatuluka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo anatulutsa khungubwi, ndipo anatuluka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa natulutsa khwangwala. Khwangwalayo ankangouluka mu mlengalenga kudikira kuti madzi aphwe pa dziko lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero natulutsa khwangwala, koma khwangwalayo ankangowuluka uku ndi uku mpaka madzi anawuma pa dziko lapansi. |
Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la chingalawa limene analipanga:
Ndipo anatulutsa njiwa imchokere, kuti aone kapena madzi anaphwa pamwamba padziko lapansi;
Ndipo kudzakhala kuti uzikamwa mumtsinje, ndipo ndalamulira makwangwala kukudyetsa kumeneko.
Ndipo makwangwala anamtengera mkate ndi nyama m'mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje.
Amkonzeratu khwangwala chakudya chake ndani, pamenepo ana ake afuulira kwa Mulungu, naulukauluka osowa chakudya?