Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziwiriziwiri za mtundu wao ulowetse m'chingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi.
Genesis 7:8 - Buku Lopatulika Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nyama zazimuna ndi zazikazi zimene anthu amaperekera nsembe, mbalame pamodzi ndi nyama zokwaŵa zomwe, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nyama zoti nʼkudya ndi nyama zosadyedwa, mbalame, pamodzi ndi nyama zokwawa zonse zinadza kwa Nowa ziwiriziwiri ndi kulowa mʼchombomo. |
Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziwiriziwiri za mtundu wao ulowetse m'chingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi.
Za mbalame monga mwa mitundu yao, ndi zinyama monga mwa mitundu yao, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ziwiriziwiri monga mwa mitundu yao, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo.
iwo, ndi zamoyo zonse monga mwa mitundu yao, ndi zinyama zonse monga mwa mitundu yao, zokwawa zonse zokwawa padziko lapansi monga mwa mitundu yao, ndi zouluka zonse monga mwa mitundu yao, ndi mbalame zonse za mitundumitundu.
Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yake; ndi nyama zosadyedwa ziwiriziwiri yamphongo ndi yaikazi yake.
Ndiponso mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbeu ikhale ndi moyo padziko lonse lapansi.
zinalowa ziwiriziwiri kwa Nowa m'chingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa.
m'menemo munali nyama za miyendo inai za mitundu yonse, ndi zokwawa za padziko ndi mbalame za m'mlengalenga.