Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 7:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Nyama zoti nʼkudya ndi nyama zosadyedwa, mbalame, pamodzi ndi nyama zokwawa zonse zinadza kwa Nowa ziwiriziwiri ndi kulowa mʼchombomo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Nyama zazimuna ndi zazikazi zimene anthu amaperekera nsembe, mbalame pamodzi ndi nyama zokwaŵa zomwe,

Onani mutuwo Koperani




Genesis 7:8
7 Mawu Ofanana  

Iwe udzalowa mʼchombocho ndi zolengedwa zamoyo zonse ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi, kuti zisungike ndi moyo pamodzi ndi iwe.


Udzatenga ziwiriziwiri za mitundu yonse ya mbalame, mitundu yonse ya nyama, ndi mitundu yonse ya zokwawa kuti zikhale ndi moyo.


Iwowa analowa mʼchombomo pamodzi ndi nyama iliyonse ya kutchire monga mwa mtundu wake, ziweto zonse monga mwa mitundu yawo, nyama yokwawa iliyonse monga mwa mtundu wake ndi mbalame iliyonse monga mwa mtundu wake.


Pa mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya utengepo zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi zazikazi zisanu ndi ziwirinso. Koma pa mtundu wa nyama iliyonse yosati nʼkudya utengepo zazimuna ziwiri ndi zazikazi ziwirinso.


Chimodzimodzinso mbalame, utenge zisanu ndi ziwiri zazimuna ndi zisanu ndi ziwiri zazikazi za mtundu uliwonse kuti mitundu yawo isungike ndi moyo pa dziko lonse lapansi.


Ndipo Nowa anatenga ziwiriziwiri, yayimuna ndi yayikazi monga anamulamulira Mulungu.


Mʼmenemo munali nyama zonse zamiyendo inayi pamodzinso ndi zokwawa za dziko lapansi ndiponso mbalame zamlengalenga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa