Ndipo chigumula chinali padziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anachuluka natukula chingalawa, ndipo chinakwera pamwamba padziko lapansi.
Genesis 7:18 - Buku Lopatulika Ndipo madzi anapambana, nachuluka ndithu padziko lapansi, ndipo chingalawa chinayandama pamadzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo madzi anapambana, nachuluka ndithu pa dziko lapansi, ndipo chingalawa chinayandama pamadzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Madziwo adanka nakwererakwerera, ndipo chombocho chidayandama pa madzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Madzi anafika mwamphamvu ndipo anachulukirachulukira pa dziko lapansi moti chombo chinayandama pamwamba pa madziwo. |
Ndipo chigumula chinali padziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anachuluka natukula chingalawa, ndipo chinakwera pamwamba padziko lapansi.
Ndipo madzi anapambana ndithu padziko lapansi; anamizidwa mapiri aatali onse amene anali pansi pathambo lonse.
Chigumula chisandifotsere, ndipo chakuya chisandimize; ndipo asanditsekere pakamwa pake pa dzenje.
Popeza madziwo anabwerera, namiza magaleta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m'nyanja; sanatsale wa iwowa ndi mmodzi yense.