Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 7:12 - Buku Lopatulika

Ndipo mvula inali padziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mvula inali pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Choncho mvula idagwa pa dziko lapansi masiku makumi anai, usana ndi usiku.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo mvula inagwa pa dziko lapansi masiku makumi anayi usana ndi usiku.

Onani mutuwo



Genesis 7:12
10 Mawu Ofanana  

Ndipo chigumula chinali padziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anachuluka natukula chingalawa, ndipo chinakwera pamwamba padziko lapansi.


Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzavumbitsa mvula padziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga padziko lapansi.


ndipo anatsekedwa akasupe a madzi aakulu ndi mazenera a kumwamba, niletsedwa mvula ya kumwamba;


Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvu ya chakudya chimenecho masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika kuphiri la Mulungu ku Horebu.


Ndipo Mose analowa m'kati mwa mtambo, nakwera m'phirimo; ndipo Mose anakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku.


Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pake anamva njala.


Ndipo ndinakhala m'phiri monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku; ndipo Yehova anandimvera ine pameneponso; Yehova sanafune kukuonongani.


Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova, monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku, osadya mkate osamwa madzi, chifukwa cha machimo anu onse mudachimwa, ndi kuchita choipacho pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.


Muja ndinakwera m'phiri kukalandira magome amiyala, ndiwo magome a chipangano chimene Yehova anapangana ndi inu, ndinakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku; osadya mkate osamwa madzi.


mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidaonongeka;