Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isaki, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe ino chaka chamawa.
Genesis 6:18 - Buku Lopatulika Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'chingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'chingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa koma iweyo ndidzachita nawe chipangano. Udzaloŵe m'chombomo iwe pamodzi ndi mkazi wako, ndi ana ako pamodzi ndi akazi ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ndidzachita pangano langa ndi iwe. Iwe, ana ako aamuna, mkazi wako ndi akazi a ana ako nonse mudzalowa mʼchombocho. |
Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isaki, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe ino chaka chamawa.
Koma Ine, taona, pangano langa lili ndi iwe, ndipo udzakhala iwe atate wa khamu la mitundu.
Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.
Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m'chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno.
Tsiku lomwelo analowa m'chingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wake wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ake pamodzi nao:
Ndipo analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m'chingalawamo, chifukwa cha madzi a chigumula.
Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.
Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.
imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka chingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;
ndipo sanalekerere dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula;