Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti, chifukwa anati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu ina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha.
Genesis 5:6 - Buku Lopatulika Ndipo Seti anakhala ndi moyo zaka zana kudza zisanu, nabala Enosi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Seti anakhala ndi moyo zaka zana kudza zisanu, nabala Enosi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Seti ali wa zaka 105, adabereka mwana dzina lake Enosi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi. |
Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti, chifukwa anati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu ina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha.
Ndiponso kwa Seti, kwa iye kunabadwa mwana wamwamuna: anamutcha dzina lake Enosi: pomwepo anthu anayamba kutchula dzina la Yehova.
Masiku ake onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anai, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira.
ndipo Seti anakhala ndi moyo, atabala Enosi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza zisanu ndi ziwiri: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi: