Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 48:3 - Buku Lopatulika

Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Adauza Yosefe kuti, “Mulungu Mphambe amene adandiwonekera ku Luzi m'dziko la Kanani, adandidalitsa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yakobo anati kwa Yosefe, “Mulungu Wamphamvuzonse anandionekera ku Luzi mʼdziko la Kanaani, ndipo anandidalitsa,

Onani mutuwo



Genesis 48:3
12 Mawu Ofanana  

Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.


Ndipo ndikubalitsa iwe ndithu, ndipo ndidzakuyesa iwe mitundu, ndipo mafumu adzatuluka mwa iwe.


Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu:


Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Taonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Israele anadzilimbitsa nakhala tsonga pakama.


Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe. Ndi madalitso a Kumwamba, madalitso a madzi akuya akukhala pansi, madalitso a mawere, ndi a mimba.


ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwike kwa iwo ndi dzina langa YEHOVA.


inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Betele, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife;


ndipo unakhala nao ulemerero wa Mulungu; kuunika kwake kunafanana ndi mwala wa mtengo wake woposa, ngati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo;


Ndipo iwo a m'nyumba ya Yosefe anatumiza ozonda ku Betele. Koma kale dzina la mzindawo ndilo Luzi.