Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 48:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yakobo anati kwa Yosefe, “Mulungu Wamphamvuzonse anandionekera ku Luzi mʼdziko la Kanaani, ndipo anandidalitsa,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Adauza Yosefe kuti, “Mulungu Mphambe amene adandiwonekera ku Luzi m'dziko la Kanani, adandidalitsa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 48:3
12 Mawu Ofanana  

Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse.


Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri motero kuti mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe. Mafumunso adzatuluka mwa iwe.


Mulungu Wamphamvuzonse akudalitse iwe nakupatse ana ambiri mpaka udzasanduke gulu lalikulu la mitundu ya anthu.


Yakobo atawuzidwa kuti, “Mwana wanu Yosefe wabwera,” Israeli anadzilimbitsa nadzuka kukhala tsonga pa bedi pake.


Chifukwa cha Mulungu wa makolo ako amene amakuthandiza; chifukwa cha Mulungu Wamphamvu, amene amakudalitsa ndi mvula yochokera kumwamba, ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka, ndipo amakudalitsa pokupatsa ana ambiri ndi ngʼombe zambiri.


Ndinaonekera kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo monga Mulungu Wamphamvuzonse, koma sindinawadziwitse dzina langa kuti ndine Yehova.


Yakobo analimbana ndi mngelo ndipo anapambana; analira napempha kuti amukomere mtima. Mulungu anakumana naye ku Beteli ndipo anayankhula naye kumeneko,


Unawala ndi ulemerero wa Mulungu, ndipo kuthwanima kwake kunali ngati mwala wamtengowapatali, ngati jasipa; woyera ngati krustalo.


Anatumiza anthu kuti akazonde Beteli. Mzindawo kale unkatchedwa Luzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa