Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake aamuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye.
Genesis 48:2 - Buku Lopatulika Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Taonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Israele anadzilimbitsa nakhala tsonga pakama. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Taonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Israele anadzilimbitsa nakhala tsonga pakama. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yakobeyo atamva kuti “Mwana wanu Yosefe wabwera kudzakuzondani,” adadzilimbitsa, nadzuka, nkukhala tsonga pabedi pompo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yakobo atawuzidwa kuti, “Mwana wanu Yosefe wabwera,” Israeli anadzilimbitsa nadzuka kukhala tsonga pa bedi pake. |
Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake aamuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye.
Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,
Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma.
Koma langiza Yoswa, numlimbitse mtima, ndi kumkhwimitsa, pakuti adzaoloka pamaso pa anthu awa, nadzawalandiritsa dziko ulionali likhale laolao.
Ndipo Yonatani mwana wa Saulo ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, namlimbitsa dzanja lake mwa Mulungu.