Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 48:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yakobo atawuzidwa kuti, “Mwana wanu Yosefe wabwera,” Israeli anadzilimbitsa nadzuka kukhala tsonga pa bedi pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Taonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Israele anadzilimbitsa nakhala tsonga pakama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Taonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Israele anadzilimbitsa nakhala tsonga pakama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Yakobeyo atamva kuti “Mwana wanu Yosefe wabwera kudzakuzondani,” adadzilimbitsa, nadzuka, nkukhala tsonga pabedi pompo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 48:2
8 Mawu Ofanana  

Patapita kanthawi Yosefe anawuzidwa kuti, “Abambo ako akudwala.” Choncho anatenga ana ake awiri aja Manase ndi Efereimu ndi kupita nawo kwa Yakobo.


Yakobo anati kwa Yosefe, “Mulungu Wamphamvuzonse anandionekera ku Luzi mʼdziko la Kanaani, ndipo anandidalitsa,


Ndinawawuza za mmene Yehova Mulungu wanga anandichitira zabwino ndiponso mawu amene mfumu inandiwuza. Tsono anati, “Tiyeni tiyambenso kumanga.” Kotero analimbitsana mtima kuti ayambenso ntchito yabwinoyi.


Yehova adzamuthandiza pamene akudwala ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.


Mwana wanga, ngati mtima wako ukhala wanzeru, inenso mtima wanga udzakondwera.


Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu.


Koma langiza Yoswa ndipo umulimbikitse ndi kumupatsa mphamvu pakuti adzatsogolera anthu awa kuwoloka ndipo adzawathandiza kuti atenge dziko limene ulioneli.”


Ndipo Yonatani mwana wa Sauli anapita kwa Davide ku Horesi ndipo anamulimbitsa mtima pomuwuza kuti Yehova ali naye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa