Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli a siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito.
Genesis 45:4 - Buku Lopatulika Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Muyandikiretu kwa ine; nayandikira. Ndipo iye anati, Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe mu Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Muyandikiretu kwa ine; nayandikira. Ndipo iye anati, Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe m'Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yosefe adaŵauza kuti, “Chonde senderani pafupi.” Onse atabwera pafupi, Yosefe adati, “Ine ndine mbale wanu uja Yosefe, amene mudamgulitsa ku Ejipito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, “Senderani pafupi nane.” Atasendera iye anati, “Ine ndine mʼbale wanu Yosefe amene munamugulitsa ku Igupto! |
Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli a siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito.
Ndiponso abale ake anamuka namgwadira pamaso pake; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu.
Ndipo makolo aakuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Ejipito; ndipo Mulungu anali naye,