Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 50:18 - Buku Lopatulika

18 Ndiponso abale ake anamuka namgwadira pamaso pake; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndiponso abale ake anamuka namgwadira pamaso pake; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Tsono abale ake adabwera nagwada pamaso pake. Adati, “Ife tili pamaso panu ngati akapolo anu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Kenaka abale ake anabwera nadzigwetsa pansi pamaso pake, nati, “Ife ndife akapolo anu.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 50:18
8 Mawu Ofanana  

Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.


ndipo anamkweza iye m'galeta wake wachiwiri amene anali naye: ndipo anafuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Ejipito.


Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.


Yudanso ndi abale ake anadza kunyumba ya Yosefe; ndipo iye akali pamenepo; ndipo anagwa pansi patsogolo pake.


Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Ine ndine Yosefe; kodi akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ake sanakhoze kumyankha iye; pakuti anavutidwa pakumuona iye.


Muziti chotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kuchimwa kwao, chifukwa kuti anakuchitirani inu choipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa akapolo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye.


Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Musaope; pakuti ndili ine kodi m'malo a Mulungu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa