Mibadwo ya Yakobo ndi iyi; Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana aamuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yao yoipa.
Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aejipito. Ndipo Yosefe anatuluka pamaso pa Farao, napitapita padziko lonse la Ejipito.