Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:46 - Buku Lopatulika

46 Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aejipito. Ndipo Yosefe anatuluka pamaso pa Farao, napitapita padziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

46 Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aejipito. Ndipo Yosefe anatuluka pamaso pa Farao, napitapita pa dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

46 Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene adayamba kugwirira ntchito Farao mfumu ya ku Ejipito. Adanyamuka, nayendera dziko lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

46 Yosefe anali ndi zaka 30 pamene amayamba ntchito kwa Farao, mfumu ya ku Igupto. Ndipo Yosefe anachoka pa maso pa Farao nayendera dziko lonse la Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:46
15 Mawu Ofanana  

Mibadwo ya Yakobo ndi iyi; Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana aamuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yao yoipa.


Ndipo zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka dzinthu nthaka inabala zambirimbiri.


Ndipo Yosefe anazindikira abale ake, koma iwo sanamzindikire iye.


Zaka ziwirizi muli njala m'dziko muno; ndipo zatsala zaka zisanu, zopanda kulima kapena kusenga.


Davide anali ndi zaka makumi atatu polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi anai.


Ndipo mfumu Rehobowamu anafunsira kwa mandoda, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake, akali moyo iyeyo, nati, Inu mundipangire bwanji kuti ndiyankhe anthu awa?


Koma iye analeka uphungu wa mandodawo, umene anampangirawo, nakafunsira kwa achinyamata anzake oimirira pamaso pake,


Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.


Ndipo mfumu inalankhula nao, koma mwa iwo onse sanapezeke monga Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya; naimirira iwo pamaso pa mfumu.


anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni.


kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito ya chihema chokomanako.


Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu.


Ndipo Yesuyo, pamene anayamba ntchito yake, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye (monga anthu adamuyesa) mwana wa Yosefe, mwana wa Eli,


Ndipo kwa Iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wake opanda chilema m'kukondwera,


Ndipo Davide anafika kwa Saulo, naima pamaso pake; ndipo iye anamkonda kwambiri, namsandutsa wonyamula zida zake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa