Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 42:11 - Buku Lopatulika

Tonse tili ana aamuna a munthu mmodzi; tili oona, akapolo anu, sitili ozonda.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Tonse tili ana amuna a munthu mmodzi; tili oona, akapolo anu, sitili ozonda.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tonsefe tili pachibale. Sindife azondi, mbuyathu, koma ndife anthu okhulupirika ndithu.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tonse ndife ana a munthu mmodzi. Ndife antchito anu okhulupirika osati akazitape.”

Onani mutuwo



Genesis 42:11
8 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anati kwa iwo, Iai, koma mwadzera kuti muone usiwa wa dziko.


Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona zili mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu.


ngati muli oona, mmodzi wa abale anu amangidwe m'kaidi momwemo; mukani inu, mupite naye tirigu wa njala ya mabanja anu;


Koma ife tinati kwa iye, Tili anthu oona; sitili ozonda;


Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? Ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?


Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.


koma m'zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja,