Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 43:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? Ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? Ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Iwo adayankha kuti, “Ndiye kuti munthuyo ankangofunsitsa za ife ndi za banja lathu nkumati, ‘Kodi bambo wanu akali moyo? Kodi muli naye mbale wanu wina?’ Tsono ife tidaayenera kuyankha mafunso onseŵa. Nanga ife tikadadziŵa bwanji kuti iye atiwuza zoti mbale wathuyo tipite naye limodzi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Iwo anayankha, “Munthuyo ankangofunsafunsa za ife ndi za banja lathu. Iye anatifunsa kuti, ‘Kodi abambo anu akanali ndi moyo? Kodi muli ndi mʼbale wanu wina?’ Ife tinkangoyankha mafunso ake. Ife tikanadziwa bwanji kuti adzanena kuti, ‘Mubwere naye kuno mʼbale wanu’?”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 43:7
6 Mawu Ofanana  

Tonse tili ana aamuna a munthu mmodzi; tili oona, akapolo anu, sitili ozonda.


Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.


Ndipo anafunsa iwo za ubwino wao, nati, Kodi atate wanu ali ndi moyo? Wokalamba uja amene munanena uja: kodi alipo?


Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.


Ndipo Israele anati, Chifukwa ninji munandichitira ine choipa chotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu?


Mbuyanga anafunsa akapolo ake kuti, Kodi muli ndi atate wanu kapena mbale wanu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa