Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 43:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo Yuda anati kwa atate wake Israele, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo Yuda anati kwa atate wake Israele, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Yuda adauza bambo wake Israele kuti, “Mnyamatayu patsani ine, ndipo tikonzeke kuti tinyamuke tizipita. Motero tonsefe, inuyo, ana athu pamodzi ndi ife, sitidzafa ndi njala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ndipo Yuda anati kwa Israeli abambo ake, “Muloleni mnyamatayo apite ndi ine, ndipo tinyamuka nthawi yomweyo, kuti ife ndi inu pamodzi ndi ana athu tikhale ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 43:8
14 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti mu Ejipito muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe.


Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.


Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tili ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng'ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye.


Ndipo ife tinati, Sitingathe kupita; mphwathu wamng'ono akakhala ndi ife, pamenepo tidzapita; pakuti sitingaone nkhope ya munthu uja, mphwathu wamng'ono akapanda kukhala ndi ife.


Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu.


Ndipo tsopano musaope; ine ndidzachereza inu, ndi ana anu aang'ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima.


ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ake, ndi mbumba ya atate wake: ang'ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng'ombe zao, anazisiya m'dziko la Goseni.


Nayankha mmodzi wa anyamata ake, nati, Atenge tsono akavalo otsala asanu, ndiwo otsala m'mudzi; taonani, adzanga unyinji wonse wa Israele otsalawo, kapena adzanga unyinji wonse wa Israele otsirizika; tiwatumize tione.


Tikati, Tilowe m'mzinda, m'mzinda muli njala, tidzafa m'mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa.


Pamenepo ndinalalikira chosala komweko kumtsinje wa Ahava, kuti tidzichepetse pamaso pa Mulungu wathu, kumfunsa ationetsere njira yolunjika ya kwa ife, ndi ang'ono athu, ndi chuma chathu chonse.


Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova.


Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.


Koma makanda anu, amene munanena za iwowa kuti adzakhala chakudya, amenewo ndidzawalowetsa, ndipo adzadziwa dzikolo mudalikana.


Rubeni akhale ndi moyo, asafe, koma amuna ake akhale owerengeka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa