Pamenepo ndinauka. Ndipo ndinaona m'kulota kwanga, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zinamera pa mbuwa imodzi zodzala ndi zabwino;
Genesis 41:23 - Buku Lopatulika ndipo, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zoonda, zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zoonda, zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pomwepo padaphukanso ngala zina zatirigu zisanu ndi ziŵiri zofwapa, zopserera ndi mphepo yakuvuma. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka panaphukanso ngala zina zisanu ndi ziwiri zofota, zowonda ndi zowauka ndi mphepo ya kummawa. |
Pamenepo ndinauka. Ndipo ndinaona m'kulota kwanga, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zinamera pa mbuwa imodzi zodzala ndi zabwino;
ndipo ngala zoonda zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino; ndipo ndinafotokozera amatsenga: koma panalibe wondimasulira ine.
Ndipo, taonani, ngala zisanu ndi ziwiri, zoonda zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao.
Chifukwa chake okhalamo ao anali ofooka manja, anaopsedwa, nachita manyazi, ananga udzu wakuthengo, ndi msipu wauwisi, ndi udzu wa patsindwi, ndi tirigu wopserera asanakule.
Chinkana abala mwa abale ake, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kuchokera kuchipululu; ndi gwero lake lidzaphwa, ndi kasupe wake adzauma, adzafunkha chuma cha akatundu onse ofunika.
Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kamvulumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzatulutsa ufa; chinkana iutulutsa, alendo adzaumeza.
Efuremu wakanthidwa, muzu wao wauma, iwo sadzabala zipatso; inde ngakhale abala, koma ndidzapha zipatso zofunika za mimba yao.