Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 9:16 - Buku Lopatulika

16 Efuremu wakanthidwa, muzu wao wauma, iwo sadzabala zipatso; inde ngakhale abala, koma ndidzapha zipatso zofunika za mimba yao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Efuremu wakanthidwa, muzu wao wauma, iwo sadzabala zipatso; inde ngakhale abala, koma ndidzapha zipatso zofunika za mimba yao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Efuremu ali ngati mtengo wodulidwa umene mizu yake yauma, ndipo sudzabalanso zipatso. Ngakhale anthuwo abale ana, ndidzaŵapha ana ao okondedwawo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Efereimu wathedwa, mizu yake yauma sakubalanso zipatso. Ngakhale atabereka ana, Ine ndidzapha ana awo okondedwawo.”

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 9:16
10 Mawu Ofanana  

ndipo, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zoonda, zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao;


Mizu yake idzauma pansi, ndi nthambi yake idzafota m'mwamba.


Inde sanaokedwe, inde sanafesedwe; inde, muzu wao sunazike pansi; koma Iye anawaombetsera mphepo, ndipo afota, ndipo kamvulumvulu awachotsa monga chiputu.


Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele.


Nena ndi nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, chokonda m'maso mwanu, chimene moyo wanu ali nacho chifundo; ndipo ana anu aamuna ndi aakazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.


Efuremu azunzika, apsinjika pa mlanduwo; pakuti anafuna mwini wake kutsata lamulolo.


Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kamvulumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzatulutsa ufa; chinkana iutulutsa, alendo adzaumeza.


Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.


Pabwalo lupanga lidzalanda, ndi m'zipinda mantha; lidzaononga mnyamata ndi namwali, woyamwa pamodzi ndi munthu waimvi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa