Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:24 - Buku Lopatulika

24 ndipo ngala zoonda zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino; ndipo ndinafotokozera amatsenga: koma panalibe wondimasulira ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 ndipo ngala zoonda zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino; ndipo ndinafotokozera amatsenga: koma panalibe wondimasulira ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Ngala zofwapazo zidameza zinzake zokhwima zija. Tsono ndidafotokozera amatsenga maloto ameneŵa, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene adatha kundimasulira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Ngala zowondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino zija. Ndinawawuza amatsenga koma palibe ndi mmodzi yemwe anatha kundimasulira.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:24
5 Mawu Ofanana  

ndipo, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zoonda, zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao;


Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a mu Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.


Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.


Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?


Pamenepo anafika alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera lotoli, koma sanandidziwitse kumasulira kwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa