Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 41:14 - Buku Lopatulika

Ndipo Farao anatumiza nakaitana Yosefe; ndipo anamtulutsa iye msanga m'dzenjemo: ndipo iye anameta, nasintha malaya ake, nalowa kwa Farao.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Farao anatumiza nakaitana Yosefe; ndipo anamtulutsa iye msanga m'dzenjemo: ndipo iye anameta, napindula malaya ake, nalowa kwa Farao.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono Farao adaitanitsa Yosefe, ndipo adamtulutsa msanga kundendeko. Iyeyo atameta bwino ndi kusintha zovala, adapita kwa Farao kuja.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Choncho Farao anamuyitanitsa Yosefe, ndipo mofulumira anabwera naye kuchokera mʼdzenje muja. Ndipo atameta, ndi kusintha zovala, anapita kwa Farao.

Onani mutuwo



Genesis 41:14
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Mefiboseti mwana wa Saulo anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasambe mapazi ake, kapena kumeta ndevu zake, kapena kutsuka zovala zake kuyambira tsiku lomuka mfumu kufikira tsiku lobwera kwao mumtendere.


Nasintha zovala zake za m'kaidi, namadya iye mkate pamaso pake masiku onse a moyo wake.


Ndipo kunali tsiku lachitatu, Estere anavala zovala zake zachifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wake wachifumu m'nyumba yachifumu, pandunji polowera m'nyumba.


Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu.


Pakuti atuluka m'nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m'dziko lake asauka.


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.


Pamenepo Ariyoki analowa naye Daniele kwa mfumu mofulumira; natero nayo, Ndapeza munthu wa ana a ndende a Yuda, ndiye adzadziwitsa mfumu kumasulira kuja.