Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 4:14 - Buku Lopatulika

14 Pakuti atuluka m'nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m'dziko lake asauka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pakuti atuluka m'nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m'dziko lake asauka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Mnyamatayo atha kukhala kuti adachita kuchokera ku ndende kudzaloŵa ufumu, kapenanso kuti adabadwa mmphaŵi m'dziko mwake momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Wachinyamatayo angathe kuchokera ku ndende ndi kudzakhala mfumu, kapena angathe kubadwa wosauka mʼdziko la mfumuyo.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 4:14
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao anatumiza nakaitana Yosefe; ndipo anamtulutsa iye msanga m'dzenjemo: ndipo iye anameta, nasintha malaya ake, nalowa kwa Farao.


Ndipo Yehoyakini mfumu ya Yuda anatulukira kwa mfumu ya Babiloni, iye ndi make, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi adindo ake; mfumu ya Babiloni nimtenga chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.


Nagona Yehoyakimu ndi makolo ake, ndipo Yehoyakini mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Napha ana a Zedekiya pamaso pake, namkolowola Zedekiya maso ake, nammanga ndi maunyolo amkuwa, namuka naye ku Babiloni.


kuika opeputsidwa pamalo ponyamuka, kuti iwo a maliro akwezedwe kosatekeseka.


Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, wachiwiri, amene adzalowa m'malo mwake.


Wodzozedwa wa Yehova, ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu, anagwidwa m'maenje ao; amene tinanena kuti, Tidzakhala m'mthunzi mwake pakati pa amitundu,


Akali m'kamwa mwa mfumu mau awa, anamgwera mau ochokera kumwamba, ndi kuti, Mfumu Nebukadinezara, anena kwa iwe: ufumu wakuchokera.


Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa