Genesis 40:7 - Buku Lopatulika Ndipo anafunsa akulu a Farao osungidwa naye m'nyumba ya mbuyake, kuti, Nkhope zanu zagwa bwanji lero? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anafunsa akulu a Farao osungidwa naye m'nyumba ya mbuyake, kuti, Nkhope zanu zagwa bwanji lero? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaŵafunsa kuti, “Mwatani mukuwoneka ngati achisoni lero?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anafunsa akuluakulu a kwa Farao amene anali naye mʼndende muja kuti, “Bwanji nkhope zanu zili zachisoni lero?” |
Nanena naye, Iwe mwana wa mfumu, uonderanji tsiku ndi tsiku? Sungandiuze kodi? Ndipo Aminoni anati kwa iye, Ndikonda Tamara, mlongo wa mbale wanga Abisalomu.
Ninena nane mfumu, Nkhope yako nja chisoni chifukwa ninji popeza sudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mtima. Pamenepo ndinachita mantha aakulu.
Ndipo anati kwa iwo, Mau awa ndi otani mulandizanawo poyendayenda? Ndipo anaima ndi nkhope zao zachisoni.
Nati iye, Mwanditengera milungu yanga ndinaipanga, ndi wansembe, ndi kuchoka; chinditsaliranso chiyani? Ndipo muneneranji kwa ine, Chakusowa nchiyani?
Ndipo mwamuna wake Elikana anati kwa iye, Hana, umaliriranji? Ndipo umakaniranji kudya? Ndipo mtima wako uwawa ninji? Ine sindili wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?