Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 13:4 - Buku Lopatulika

4 Nanena naye, Iwe mwana wa mfumu, uonderanji tsiku ndi tsiku? Sungandiuze kodi? Ndipo Aminoni anati kwa iye, Ndikonda Tamara, mlongo wa mbale wanga Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Nanena naye, Iwe mwana wa mfumu, uonderanji tsiku ndi tsiku? Sungandiuze kodi? Ndipo Aminoni anati kwa iye, Ndikonda Tamara, mlongo wa mbale wanga Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsiku lina Yonadabu adafunsa Aminoni kuti, “Kodi iwe, mwana wa mfumu, chifukwa chiyani umaoneka woonda m'maŵa masiku onse? Bwanji osandiwuza ine?” Aminoni adamuyankha kuti, “Ine ndikukonda Tamara, mlongo wa mkulu wanga Abisalomu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Iye anafunsa Amnoni, “Nʼchifukwa chiyani iwe mwana wa mfumu, umaoneka wowonda mmawa uliwonse? Bwanji wosandiwuza?” Amnoni anamuyankha kuti, “Ine ndamukonda Tamara, mlongo wa mʼbale wanga Abisalomu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:4
11 Mawu Ofanana  

Koma Aminoni anali ndi bwenzi lake, dzina lake ndiye Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide. Ndipo Yonadabu anali munthu wochenjera ndithu.


Ndipo Yonadabu ananena naye, Ugone pa kama wako ndi kudzikokomera ulikudwala; ndipo pamene atate wako akadzakuona unene naye, Mulole mlongo wanga Tamara abwere kundipatsa kudya, nakonzere chakudyacho pamaso panga kuti ndichione ndi kuchidya cha m'manja mwake.


Koma Yezebele mkazi wake anadza kwa iye, nati kwa iye, Muchitiranji msunamo, kuti mukana kudya mkate?


Ndipo Yezebele mkazi wake anati kwa iye, Kodi mulamulira Aisraele tsopano ndinu? Taukani, idyani mkate, ukondwere mtima wanu; munda wa Naboti wa ku Yezireele ndidzakupatsani ndine.


Maonekedwe a nkhope zao awachitira iwo mboni; ndipo amaonetsa uchimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! Chifukwa iwo anadzichitira zoipa iwo okha.


Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.


Usamavula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina.


Munthu akatenga mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, nakaona thupi lake, ndi mlongoyo akaona thupi lake; chochititsa manyazi ichi; ndipo awasadze pamaso pa ana a anthu ao; anavula mlongo wake; asenze mphulupulu yake.


Manja ao onse awiri agwira choipa kuchichita ndi changu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphotho; ndi wamkuluyo angonena chosakaza moyo wake; ndipo achiluka pamodzi.


Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa