Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Ejipito; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, Mwejipito, anamgula iye m'manja mwa Aismaele amene anatsika naye kunka kumeneko.
Genesis 40:3 - Buku Lopatulika Ndipo anaika iwo asungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, m'kaidi, umo anamangidwa Yosefe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaika iwo asungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, m'kaidi, umo anamangidwa Yosefe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero adaŵatsekera m'ndende, nakaŵaika m'manja mwa mkulu wa asilikali olonda kunyumba kwa mfumu uja, m'ndende momwe Yosefe ankasungidwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anakawatsekera mʼndende, nakawayika mʼmanja mwa mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa mfumu kuja, mʼndende momwe Yosefe ankasungidwamo. |
Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Ejipito; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, Mwejipito, anamgula iye m'manja mwa Aismaele amene anatsika naye kunka kumeneko.
Ndipo mbuyake wa Yosefe anamtenga iye namuika m'kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m'mwemo m'kaidimo.
Ndipo woyang'anira kaidi anapereka m'manja a Yosefe akaidi onse okhala m'kaidimo, ndipo zonse iwo anazichita m'menemo, iye ndiye wozichita.
Woyang'anira m'kaidi sanayang'anire kanthu kalikonse kamene kanali m'manja a Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi iye; ndipo zimene anazichita, Yehova anazipindulitsa.
Ndipo kazembe wa alonda anapereka iwo kwa Yosefe, ndipo iye anawatumikira iwo: ndipo anakhala nthawi mosungidwamo.
Farao anakwiya ndi anyamata ake, nandiika ine ndisungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, ine ndi wophika mkate wamkulu: