Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 39:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Ejipito; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, Mwejipito, anamgula iye m'manja mwa Aismaele amene anatsika naye kunka kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Ejipito; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, Mwejipito, anamgula iye m'manja mwa Aismaele amene anatsika naye kunka kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Aismaele aja adapita naye Yosefe ku Ejipito kumene Potifara Mwejipito, nduna ya Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda kunyumba ya mfumu, adamgula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsopano Yosefe anatengedwa kupita ku Igupto. Potifara Mwigupto amene anali mmodzi wa akuluakulu a Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa Farao, anagula Yosefe kwa Aismaeli amene anapita naye kumeneko.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 39:1
7 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismaele anachokera ku Giliyadi ndi ngamira zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi mure alinkumuka kutsikira nazo ku Ejipito.


Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli a siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito.


Amidiyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Ejipito kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.


Ndipo anaika iwo asungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, m'kaidi, umo anamangidwa Yosefe.


Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Muyandikiretu kwa ine; nayandikira. Ndipo iye anati, Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe mu Ejipito.


Anawatsogozeratu munthu; anamgulitsa Yosefe akhale kapolo:


Ndipo makolo aakuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Ejipito; ndipo Mulungu anali naye,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa