Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 40:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 ndipo anakawatsekera mʼndende, nakawayika mʼmanja mwa mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa mfumu kuja, mʼndende momwe Yosefe ankasungidwamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo anaika iwo asungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, m'kaidi, umo anamangidwa Yosefe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo anaika iwo asungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, m'kaidi, umo anamangidwa Yosefe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Motero adaŵatsekera m'ndende, nakaŵaika m'manja mwa mkulu wa asilikali olonda kunyumba kwa mfumu uja, m'ndende momwe Yosefe ankasungidwa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 40:3
6 Mawu Ofanana  

Tsopano Yosefe anatengedwa kupita ku Igupto. Potifara Mwigupto amene anali mmodzi wa akuluakulu a Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa Farao, anagula Yosefe kwa Aismaeli amene anapita naye kumeneko.


Tsono iye anatenga Yosefe namuyika mʼndende mmene ankasungiramo amʼndende a mfumu. Ndipo Yosefe anakhala mʼndendemo


Choncho woyangʼanira ndende uja anamuyika Yosefe kukhala woyangʼanira onse amene anayikidwa mʼndende. Ndiponso anamupatsa udindo woyangʼanira zonse zochitika mʼndendemo.


Woyangʼanira ndende uja sankayangʼaniranso china chilichonse chimene chinali mu ulamuliro wa Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi Yosefe. Ndipo Yehova anaonetsetsa kuti chilichonse chimene Yosefe ankachita chimuyendere bwino.


Mkulu wa alonda aja anawapereka mʼmanja mwa Yosefe, ndipo iye anawasamalira. Iwo anakhala mʼndendemo kwa kanthawi.


Paja nthawi ina Farao anapsera mtima antchito akefe, ndipo anatitsekera (ine ndi mkulu wa ophika buledi) mʼndende, mʼnyumba ya mkulu wa alonda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa