ndipo chikho cha Farao chinali m'dzanja langa: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m'chikho cha Farao ndi kupereka chikho m'dzanja la Farao.
Genesis 40:12 - Buku Lopatulika Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yosefe adamuyankha kuti, “Tanthauzo lake la maloto ameneŵa nali: nthambi zitatuzo ndi masiku atatu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yosefe anati kwa iye, “Tanthauzo lake ndi ili: Nthambi zitatuzo ndi masiku atatu. |
ndipo chikho cha Farao chinali m'dzanja langa: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m'chikho cha Farao ndi kupereka chikho m'dzanja la Farao.
akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako; ndipo udzapereka chikho cha Farao m'dzanja lake, monga kale lomwe m'mene unali wopereka chikho chake.
Ndipo Yosefe anayankha nati, Kumasulira kwake ndi uku: malichero atatu ndiwo masiku atatu;
Ndipo panali ndi ife mnyamata Muhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga loto lake anatimasulira.
Ichi ndi chinthu chimene ndinena kwa Farao: chimene Mulungu ati achite wasonyeza kwa Farao.
Loto ili ndinaliona ine mfumu Nebukadinezara; ndipo iwe, Belitesazara, undifotokozere kumasulira kwake, popeza anzeru onse a mu ufumu wanga sangathe kundidziwitsa kumasulira kwake; koma iwe ukhoza, popeza mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera.
Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa.
namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Khristu.
Koma Hagara ndiye phiri la Sinai, mu Arabiya, nafanana ndi Yerusalemu wa tsopano; pakuti ali muukapolo pamodzi ndi ana ake.
Ndipo mnzake anayankha nati, Ichi si china konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yowasi, munthu wa Israele; Mulungu wapereka Midiyani ndi a m'misasa onse m'dzanja lake.