Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 4:18 - Buku Lopatulika

18 Loto ili ndinaliona ine mfumu Nebukadinezara; ndipo iwe, Belitesazara, undifotokozere kumasulira kwake, popeza anzeru onse a mu ufumu wanga sangathe kundidziwitsa kumasulira kwake; koma iwe ukhoza, popeza mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Loto ili ndinaliona ine mfumu Nebukadinezara; ndipo iwe, Belitesazara, undifotokozere kumasulira kwake, popeza anzeru onse a m'ufumu wanga sakhoza kundidziwitsa kumasulira kwake; koma iwe ukhoza, popeza mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 “Amenewa ndi maloto amene ine, mfumu Nebukadinezara, ndinalota. Tsopano Belitesezara, undifotokozere tanthauzo lake, popeza palibe mwa anthu anzeru a mu ufumu wanga amene angathe kunditanthauzira. Koma iwe ukhoza, chifukwa mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe.”

Onani mutuwo Koperani




Danieli 4:18
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu;


Farao ndipo anati kwa Yosefe, Ine ndalota loto, koma palibe wondimasulira; ndipo ndamva alikunena za iwe kuti, ukamva loto udziwa kumasulira.


Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a mu Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.


Ndipo mzimu wa Ejipito adzakhala wachabe pakati pake; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wake; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.


Ndipo m'mau ali onse anzeru ndi aluntha, amene mfumu inawafunsira. Inawapeza akuposa alembi ndi openda onse mu ufumu wake wonse.


ndipo paliponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga, m'dzanja lanu; nakuchititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolide.


Nabwerezanso iwo kuyankha, nati, Mfumu ifotokozere anyamata ake lotoli, ndipo tidzaidziwitsa kumasulira kwake.


Ndipo tsono anabwera nao kwa ine anzeru, openda, kuti awerenge lemba ilo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake; koma sanakhoze kufotokozera kumasulira kwa chinthuchi.


Pamenepo analowa anzeru onse a mfumu, koma sanakhoze kuwerenga lembalo, kapena kudziwitsa mfumu kumasulira kwake.


Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa