Wathawanji iwe mobisika, ndi kundichokera kuseri, osandiuza ine, kuti ndikadakumukitsa iwe ndi kusekerera ndi nyimbo ndi lingaka ndi zeze?
Genesis 4:21 - Buku Lopatulika Ndi dzina la mphwake ndilo Yubala; iye ndiye atate wao wa iwo oimba zeze ndi chitoliro. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi dzina la mphwake ndilo Yubale; iye ndiye atate wao wa iwo oimba zeze ndi chitoliro. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbale wake anali Yubale, ndipo ndiye kholo la onse okhoza kuimba zeze ndi toliro. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzina la mʼbale wake linali Yubala; iyeyu anali kholo la onse oyimba zeze ndi chitoliro. |
Wathawanji iwe mobisika, ndi kundichokera kuseri, osandiuza ine, kuti ndikadakumukitsa iwe ndi kusekerera ndi nyimbo ndi lingaka ndi zeze?
Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a chitsulo; mlongo wake wa Tubala-Kaini ndi Naama.
Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro.
Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m'maphwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa machitidwe a manja ake.