Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 31:27 - Buku Lopatulika

27 Wathawanji iwe mobisika, ndi kundichokera kuseri, osandiuza ine, kuti ndikadakumukitsa iwe ndi kusekerera ndi nyimbo ndi lingaka ndi zeze?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Wathawanji iwe mobisika, ndi kundichokera kuseri, osandiuza ine, kuti ndikadakumukitsa iwe ndi kusekerera ndi nyimbo ndi lingaka ndi zeze?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Chifukwa chiyani wandinyenga ndi kundizemba osandiwuza? Ukadandiwuza, bwenzi nditakulola mokondwa, ndipo bwenzi pali kumaimba nyimbo ndi ting'oma ndi azeze.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Chifukwa chiyani unandinamiza ndi kuthawa mozemba wosandiwuza? Ukanandiwuza, bwezi titatsanzikana mwa chisangalalo ndi kuyimba nyimbo ndi zisekese ndi azeze.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:27
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wachitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga aakazi, monga mikoli ya lupanga.


Ndipo anayankha Yakobo nati kwa Labani, Chifukwa ndinaopa: chifukwa kuti, ndinati, Kapena udzandilanda ine ana ako aakazi.


Ndi dzina la mphwake ndilo Yubala; iye ndiye atate wao wa iwo oimba zeze ndi chitoliro.


Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.


Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m'maphwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa machitidwe a manja ake.


Pamenepo Gideoni anatenga amuna khumi mwa anyamata ake, nachita monga Yehova adanena naye; ndipo kunali, popeza anaopa akunyumba ya atate wake, ndi amuna akumudziwo, sanachichite msana, koma usiku.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa