Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.
Genesis 4:17 - Buku Lopatulika Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wake; ndipo anatenga pakati, nabala Enoki: ndipo anamanga mzinda, nautcha dzina lake la mzindawo monga dzina la mwana wake, Enoki. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wake; ndipo anatenga pakati, nabala Enoki: ndipo anamanga mudzi, nautcha dzina lake la mudziwo monga dzina la mwana wake, Enoki. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kaini adakhala ndi mkazi wake, mkaziyo adatenga pathupi, nabala mwana dzina lake Enoki. Tsono Kaini adamanga mzinda, nautcha dzina la mwana wake Enoki. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kaini anagona malo amodzi ndi mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Enoki. Kaini nthawi imeneyo nʼkuti akumanga mzinda ndipo anawutcha dzina la mwana wake Enoki. |
Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.
Ndipo Kaini anatuluka pamaso pa Yehova, ndipo anakhala m'dziko la Nodi, kum'mawa kwake kwa Edeni.
Kwa Enoki ndipo kunabadwa Iradi; Iradi ndipo anabala Mehuyaele; Mehuyaele ndipo anabala Metusaele; Metusaele ndipo anabala Lameki.
Ndipo Yaredi anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri, nabala Enoki;
ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi;
Koma Abisalomu akali moyo adatenga nadziutsira choimiritsacho chili m'chigwa cha mfumu; pakuti anati, Ndilibe mwana wamwamuna adzakhala chikumbutso cha dzina langa; natcha choimiritsacho ndi dzina la iye yekha; ndipo chitchedwa chikumbutso cha Abisalomu, kufikira lero lomwe.
Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala chikhalire, ndi mokhala iwo ku mibadwomibadwo; atchapo dzina lao padziko pao.
Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wachifumu wanga?