Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 49:11 - Buku Lopatulika

11 Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala chikhalire, ndi mokhala iwo ku mibadwomibadwo; atchapo dzina lao padziko pao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala chikhalire, ndi mokhala iwo ku mibadwomibadwo; atchapo dzina lao padziko pao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Manda ao ndiye kwao mpaka muyaya, ndi malo odzakhalako pa mibadwo yonse, ngakhale akadali moyo ankatcha maiko maina ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya, malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo, ngakhale anatchula malo mayina awo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 49:11
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wake; ndipo anatenga pakati, nabala Enoki: ndipo anamanga mzinda, nautcha dzina lake la mzindawo monga dzina la mwana wake, Enoki.


Koma Abisalomu akali moyo adatenga nadziutsira choimiritsacho chili m'chigwa cha mfumu; pakuti anati, Ndilibe mwana wamwamuna adzakhala chikumbutso cha dzina langa; natcha choimiritsacho ndi dzina la iye yekha; ndipo chitchedwa chikumbutso cha Abisalomu, kufikira lero lomwe.


Ati mumtima mwake, Sindidzagwedezeka ine; ku mibadwomibadwo osagwa m'tsoka ine.


Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira chiyani? Chiyembekezo changa chili pa Inu.


Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika; m'kati mwao m'mosakaza; m'mero mwao ndi manda apululu; lilime lao asyasyalika nalo.


Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi mpaka kutha; chingakhale cha m'kati mwake mwa munthu, ndi mtima wozama.


Wanzeru maso ake ali m'mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.


Pakuti pali munthu wina agwira ntchito mwanzeru ndi modziwa nadzipinduliramo; koma adzapereka gawo lake kwa munthu amene sanagwirepo ntchito. Ichinso ndi chabe ndi choipa chachikulu.


Atero Ambuye Yehova, Kudzachitika tsiku ilo kuti m'mtima mwako mudzalowa zinthu, nudzalingirira chiwembu choipa,


Koma Ambuye anati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m'kati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa.


Chifukwa chake lapa choipa chako ichi, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe cholingirira cha mtima wako.


Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobu, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalitcha dzina lake, Basani Havoti-Yairi, kufikira lero lino).


Ndipo Samuele analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Saulo; ndipo munthu anamuuza Samuele kuti, Saulo anafika ku Karimele, ndipo taonani, anaimika chikumbutso chake, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa