Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 49:10 - Buku Lopatulika

10 Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Zoonadi, aliyense atha kuwona kuti ngakhale anthu anzeru amafa. Chimodzimodzi, anthu opusa ndi opulukira ayenera kufa ndi kusiyira ena chuma chao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira; opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 49:10
21 Mawu Ofanana  

kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.


Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?


pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse; ulemu wake sutsika naye kumtsata m'mbuyo.


ndinali wam'thengo, wosadziwa kanthu; ndinali ngati nyama pamaso panu.


Chilikuti chifundo chanu chakale, Ambuye, munachilumbirira Davide pa chikhulupiriko chanu?


Zindikirani, opulukira inu mwa anthu; ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti?


Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.


Wokonda mwambo akonda kudziwa; koma wakuda chidzudzulo apulukira.


Korona wa anzeru ndi chuma chao; utsiru wa opusa ndiwo utsiru.


pakuti ndipambana anthu onse kupulukira, ndilibe luntha la munthu.


Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo chilangizo, chopanda pake.


Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikire, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa.


Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?


Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa