Ndipo panali, nthawi yomweyo, iye analowa m'nyumba kuti agwire ntchito yake; ndipo munalibe amuna a m'nyumba m'katimo.
Genesis 39:10 - Buku Lopatulika Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvere mkazi kugona naye kapena kukhala naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvere mkazi kugona naye kapena kukhala naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngakhale mkazi uja ankalankhula mau ameneŵa kwa Yosefe tsiku ndi tsiku, Yosefeyo sankamvako mpang'ono pomwe, ndipo sankalola kuchita naye zoipa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ngakhale kuti iye anayankhula mawu omwewa ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, Yosefe sanalole kugona naye ngakhale kukhala naye pafupi. |
Ndipo panali, nthawi yomweyo, iye analowa m'nyumba kuti agwire ntchito yake; ndipo munalibe amuna a m'nyumba m'katimo.
Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyake, Taonani, mbuyanga sadziwa chimene chili ndi ine m'nyumbamu, ndipo anaika zake zonse m'manja anga;
mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?
Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake;
Pakuti mkazi wadama ndiye dzenje lakuya; ndipo mkazi wachiwerewere ndiye mbuna yopapatiza.
Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere ikukha uchi; m'kamwa mwake muti see koposa mafuta.
Kuti zikutchinjirizire kwa mkazi wachiwerewere, kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ake.
Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.
Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye aang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira;
Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.
Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;