Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 5:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere ikukha uchi; m'kamwa mwake muti see koposa mafuta.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere ikukha uchi; m'kamwa mwake muti see koposa mafuta.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Paja mkazi wadama ali ndi pakamwa pokoma ngati uchi, mau ake ndi osalala koposa mafuta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi. Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta,

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 5:3
10 Mawu Ofanana  

Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.


Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake;


M'kamwa mwa mkazi wachiwerewere muli dzenje lakuya; yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo.


Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi wachiwerewere, ndi kufungatira chifuwa cha mkazi wachilendo?


Zikutchinjiriza kwa mkazi woipa, ndi kulilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere.


Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ake, ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake.


Kuti zikutchinjirizire kwa mkazi wachiwerewere, kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ake.


ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.


M'milomo yako, mkwatibwi, mukukha uchi, uchi ndi mkaka zili pansi pa lilime lako; kununkhira kwa zovala zako ndi kunga kununkhira kwa Lebanoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa