Genesis 30:6 - Buku Lopatulika Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; chifukwa chake anamutcha dzina lake Dani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; chifukwa chake anamutcha dzina lake Dani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Rakele adati, “Mulungu waweruza mondikomera mtima. Wamva pemphero langa, ndipo wandipatsa mwana wamwamuna.” Motero mwanayo adamutcha Dani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Rakele anati, “Mulungu waweruza mondikomera mtima, wamva kupempha kwanga ndipo wandipatsa mwana wa mwamuna.” Choncho anamutcha Dani. |
Ndipo Biliha mdzakazi wake wa Rakele anatenganso pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiwiri.
Mundiweruze monga mwa chilungamo chanu, Yehova Mulungu wanga; ndipo asandisekerere ine.
Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.
A ana a Dani, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Naimirire awa paphiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Asere, ndi Zebuloni, Dani ndi Nafutali.