Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wake, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake.
Genesis 30:3 - Buku Lopatulika Ndipo Rakele anati, Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Rakele anati, Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Rakele adati, “Nayu mdzakazi wanga Biliha, khala nayeni kuti andibalire mwana. Motere podzera mwa iye, inenso ndidzakhala ndi ana.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Rakele anati kwa Yakobo, “Mdzakazi wanga Biliha nayu. Lowana naye kuti mwina nʼkundibalira mwana, ndipo kudzera mwa iyeyu nanenso nʼkukhala ndi ana.” |
Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wake, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake.
Amenewa ndi ana a Biliha, amene Labani anampatsa Rakele mwana wake wamkazi, amenewo anambalira Yakobo; anthu onse ndiwo asanu ndi awiri.
Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.
Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera mu Efurata, numveke mu Betelehemu;